Levitiko 16:4 - Buku Lopatulika4 Avale malaya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zovala za kumiyendo pathupi pake, nadzimangire m'chuuno ndi mpango wabafuta, navale nduwira yabafuta; izi ndi zovala zopatulika; potero asambe thupi lake ndi madzi, ndi kuvala izi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Avale malaya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zovala za kumiyendo pathupi pake, nadzimangire m'chuuno ndi mpango wabafuta, navale nduwira yabafuta; izi ndi zovala zopatulika; potero asambe thupi lake ndi madzi, ndi kuvala izi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Azivala mwinjiro woyera wabafuta, azivalanso kabudula wabafuta ndi kumangira lamba wabafuta, ndipo avalenso nduŵira yabafuta kumutu. Zimenezi ndi zovala zopatulika. Avale zimenezi atasamba thupi lonse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Azivala mwinjiro wopatulika wa nsalu yosalala, azivalanso kabudula wa mʼkati wa nsalu yosalala, azimanga lamba wa nsalu yosalala, ndipo avalenso nduwira ya nsalu yosalala kumutu. Zimenezi ndi nsalu zopatulika ndipo atasamba thupi lonse azivala zimenezi. Onani mutuwo |