Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 10:9 - Buku Lopatulika

9 Usamamwa vinyo, kapena choledzeretsa, iwe ndi ana ako omwe, m'mene mulowa m'chihema chokomanako, kuti mungafe; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Usamamwa vinyo, kapena choledzeretsa, iwe ndi ana ako omwe, m'mene mulowa m'chihema chokomanako, kuti mungafe; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Usamwe vinyo kapena chakumwa china champhamvu, iwe ndi ana ako uli nawoŵa, pamene mukupita ku chihema chamsonkhano, kuwopa kuti mungafe. Limeneli likhale lamulo losatha pa mibadwo yanu yonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Iwe ndi ana ako musamamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa pamene mukulowa mu tenti ya msonkhano kuti mungafe. Ili ndi lamulo lamuyaya pa mibado yanu yonse.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 10:9
17 Mawu Ofanana  

Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.


Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru.


Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi chakumwa chaukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, adzandima popenya, naphunthwa poweruza.


Kungakhale kumwa vinyo, wansembe asamwe polowa kubwalo la m'katimo.


Chigololo, ndi vinyo, ndi vinyo watsopano, zichotsa mtima.


Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, nati,


Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.


ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ichi nchopatulikira wansembe, pamodzi ndi nganga ya nsembe yoweyula, pamodzi ndi mwendo wa nsembe yokweza; ndipo atatero Mnaziri amwe vinyo.


azisala vinyo ndi kachasu; asamwe vinyo wosasa, kapena kachasu wosasa, kapena chakumwa chonse cha mphesa, asamwe; asadye mphesa zaziwisi kapena zouma.


Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena kachasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.


Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu,


wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba chuma;


Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a chisiriro chonyansa;


Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu uchite naye vinyo pang'ono, chifukwa cha mimba yako ndi zofooka zako zobwera kawirikawiri.


Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa