Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 10:10 - Buku Lopatulika

10 ndi kuti musiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi pakati pa zodetsedwa ndi zoyera;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 ndi kuti musiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi pakati pa zodetsedwa ndi zoyera;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Muzisiyanitsa pakati pa zinthu zoyera ndi zinthu wamba, ndiponso pakati pa zinthu zonyansa ndi zinthu zoyenera pa zachipembedzo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Muzisiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba, pakati pa zinthu zodetsedwa ndi zinthu zoyeretsedwa,

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 10:10
9 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake atero Yehova, Ukabwerera pamenepo ndidzakubwezanso, kuti uime pamaso panga; ndipo ukasiyanitsa cha mtengo wake ndi chonyansa, udzakhala ngati m'kamwa mwanga; ndipo adzabwerera kwa iwe, koma sudzabwerera kwa iwo.


Ansembe ake achitira choipa chilamulo changa, nadetsa zopatulika zanga, sasiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndipo sazindikiritsa anthu pakati pa zodetsa ndi zoyera, nabisira masabata anga maso ao; ndipo Ine ndidetsedwa pakati pao.


Ndipo aziphunzitsa anthu anga asiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi kuwazindikiritsa pakati pa zodetsa ndi zoyera.


kusiyanitsa pakati zodetsa ndi zoyera, ndi pakati pa zamoyo zakudya ndi zamoyo zosadya.


Pamenepo wansembe azimuona, ndipo taonani, ngati chotupa chake cha nthenda chili chotuuluka pa dazi la pamutu wake, kapena la pamphumi pake, monga maonekedwe a khate pa khungu la thupi;


kulangiza tsiku loti chikhala chodetsa, ndi tsiku loti chikhala choyera; ichi ndi chilamulo cha khate.


Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupirira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi chikumbumtima chao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa