Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 1:9 - Buku Lopatulika

9 koma atsuke ndi madzi matumbo ake ndi miyendo yake; ndi wansembe atenthe zonsezi paguwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 koma atsuke ndi madzi matumbo ake ndi miyendo yake; ndi wansembe atenthe zonsezi pa guwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma atsuke matumbo ake pamodzi ndi miyendo yake yomwe. Tsono wansembe aipsereze nyama yathunthuyo pa guwa, kuti ikhale nsembe yopsereza, yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Munthuyo atsuke zamʼkati mwa nyamayo pamodzi ndi miyendo yake yomwe, ndipo wansembe awotche nyama yonse paguwapo. Iyi ndi nsembe yopsereza, chopereka chowotcha pa moto, cha fungo lokomera Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 1:9
35 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.


mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu, mwana wa Eliyele, mwana wa Towa,


Anapanganso mbiya zaphwamphwa khumi, naika zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere, kutsukiramo; za nsembe yopsereza anazitsuka m'menemo; koma thawale ndi la ansembe kusambiramo.


Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo; ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru.


Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona, pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa; ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi.


Musaidya yaiwisi, kapena yophika ndi madzi konse ai, koma yoocha pamoto; mutu wake ndi miyendo yake ndi matumbo ake.


Pamenepo upsereze nkhosa yamphongo yonse paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.


Pamenepo uzilandire m'manja mwao, ndi kuzipsereza paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zichite fungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.


Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?


Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.


Ngati fungo lokoma ndidzakulandirani pakukutulutsani mwa mitundu ya anthu, ndipo ndidzakusonkhanitsani kukuchotsani m'maiko munabalalikiramo, ndipo ndidzazindikirika Woyera mwa inu pamaso pa amitundu.


Ndipo pa nsanamira za pazipata panali kanyumba ndi chitseko chake; pamenepo anatsuka nsembe yopsereza.


Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


nang'ambe mapiko ake osawachotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe paguwa la nsembe, pa nkhuni zili pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo wansembe atenthe chikumbutso chake, atatapa pa tirigu wake wokonola, ndi pa mafuta ake, ndi kutenga lubani lake lonse; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.


Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi lubani wake wonse; ndipo wansembeyo aitenthe chikumbutso chake paguwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo wansembeyo atengeko chikumbutso pa nsembe yaufa, nachitenthe paguwa la nsembe; ndicho nsembe yamoto ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo wansembe azitenthe paguwa la nsembe; ndicho chakudya cha nsembe yamoto ya kwa Yehova.


Ndipo ana a Aroni azitenthe paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, ili pa nkhuni zimene zili pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Nachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe paguwa la nsembe akhale fungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.


Ndipo chilamulo cha chopereka chaufa ndicho: ana a Aroni azibwera nacho pamaso pa Yehova ku guwa la nsembe.


Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.


Pamenepo Mose anazichotsa ku manja ao, nazitentha paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza; ndizo nsembe zodzaza manja zochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.


Ndipo anatsuka matumbo ndi miyendo, nazitentha pa nsembe yopsereza paguwa la nsembe.


Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.


ndipo mukakonzera Yehova nsembe yamoto, nsembe yopsereza, kapena yophera, pochita chowinda cha padera, kapena nsembe yaufulu, kapena nsembe ya pa nyengo zanu zoikika, kumchitira Yehova fungo lokoma, la ng'ombe kapena nkhosa;


Ndipo poyamba miyezi yanu muzibwera nayo nsembe yopsereza ya Yehova: ng'ombe zamphongo ziwiri, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema;


Ndi nsembe yake yothira ya mwanawankhosa mmodziyo ndiyo limodzi la magawo anai la hini; m'malo opatulika uthirire Yehova nsembe yothira ya chakumwa cholimba.


Ndi mwanawankhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m'mawa, ndi nsembe yothira yake, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova.


Pakuti ife ndife fungo labwino la Khristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena fungo la imfa kuimfa;


ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.


ndipo mupereke nsembe zanu zopsereza, nyama zao ndi mwazi wao, paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu; ndipo athire mwazi wa nsembe zanu zophera paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyama yake muidye.


Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa