Hoseya 9:7 - Buku Lopatulika7 Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israele adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, chifukwa cha kuchuluka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israele adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, chifukwa cha kuchuluka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Nthaŵi ya chilango yafikadi, masiku olipsira aŵagwera. Pamenepo adzadziŵa kuti zimenezi nzoonadi. Tsopano akunena kuti, “Mneneriyu nchitsilu, munthu wa nzeru za kwa Mulunguyu ndi wamsala!” Amatero chifukwa zolakwa zao zachuluka, chidani chao nchachikulukulu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Masiku achilango akubwera, masiku obwezera ali pafupi. Israeli adziwe zimenezi. Chifukwa machimo anu ndi ochuluka kwambiri ndipo udani wanu pa Mulungu ndi waukulu kwambiri. Mneneri amamuyesa chitsiru, munthu wanzeru za kwa Mulungu ngati wamisala. Onani mutuwo |