Hoseya 9:6 - Buku Lopatulika6 Pakuti taonani, anachokera chionongeko, koma Ejipito adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m'manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m'mahema mwao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Pakuti taonani, anachokera chionongeko, koma Ejipito adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m'manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m'mahema mwao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Nthaŵi ya chilango ikadzafika, iwo nkubalalika, Aejipito adzaŵakusa, nakaŵaika m'manda komweko ku Memfisi. Khwisa adzamera pa ziŵiya zao zasiliva. M'nyumba mwao mudzamera minga. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Ngakhale iwo atathawa chiwonongeko, Igupto adzawasonkhanitsa, ndipo Mefisi adzawayika mʼmanda. Khwisa adzamera pa ziwiya zawo zasiliva, ndipo minga idzamera mʼmatenti awo. Onani mutuwo |
Ndipo ndidzatenga otsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Ejipito akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Ejipito adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo.