Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 8:9 - Buku Lopatulika

9 Pakuti anakwera kunka ku Asiriya, ngati mbidzi ya pa yokha mwini wake; Efuremu walembera omkonda ngati antchito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pakuti anakwera kunka ku Asiriya, ngati mbidzi ya pa yokha mwini wake; Efuremu walembera omkonda ngati antchito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Adathaŵira ku Asiriya ngati mbidzi yongodziyendera payokha. Aefuremu adalipira anthu a ku maiko ena kuti akhale oŵathandiza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Pakuti iwo anapita ku Asiriya ngati mbidzi yongodziyendera pa yokha. Efereimu wadzigulitsa kwa zibwenzi zake.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 8:9
13 Mawu Ofanana  

Pamenepo Pulo mfumu ya Asiriya anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Pulo matalente a siliva chikwi chimodzi; kuti dzanja lake likhale naye kukhazikitsa ufumu m'dzanja lake.


amene ayenda kutsikira ku Ejipito, osafunsa kukamwa kwanga, kudzilimbitsa iwo okha ndi mphamvu za Farao, ndi kukhulupirira mthunzi wa Ejipito!


Katundu wa zilombo za kumwera. M'dziko lovuta ndi lopweteka, kumeneko kuchokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula chuma chao pamsana pa abulu, ndi ang'ono zolemera zao pa malinundu a ngamira, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao.


mbidzi yozolowera m'chipululu, yopumira mphepo pakufuna pake; pokomana nayo ndani adzaibweza? Onse amene aifuna sadzadzilemetsa; adzaipeza m'mwezi wake.


Efuremu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse achulukitsa mabodza ndi chipasuko, ndipo achita pangano ndi Asiriya, natenga mafuta kunka nao ku Ejipito.


Ndipo Yehova ali ndi mlandu ndi Yuda, nadzalanga Yakobo monga mwa njira zake, adzambwezera monga mwa machitidwe ake.


Ndipo tsopano ndidzaonetsa manyazi ake pamaso pa omkonda, popandanso wakumlanditsa m'dzanja langa.


Pamene Efuremu anaona nthenda yake, ndi Yuda bala lake, Efuremu anamuka kwa Asiriya, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuchiritsani, kapena kupoletsa bala lanu.


Ndipo Efuremu ali ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru; aitanira kwa Ejipito, amuka kwa Asiriya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa