Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 8:6 - Buku Lopatulika

6 Pakuti ichi chomwe chafumira kwa Israele; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwanawang'ombe wa Samariya adzaphwanyikaphwanyika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Pakuti ichi chomwe chafumira kwa Israele; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwanawang'ombe wa Samariya adzaphwanyikaphwanyika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 “Fanolo si mulungu konse, adalipanga ndi munthu waluso. Fano la ku Samariyali lidzatswanyidwa pafupipafupi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Mafanowa ndi ochokera ku Israeli! Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso; si Mulungu amene anamupanga. Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa, mwana wangʼombe wa ku Samariya.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 8:6
22 Mawu Ofanana  

Anagumulanso guwa la nsembe linali ku Betele, ndi msanje adaumanga Yerobowamu mwana wa Nebati wolakwitsa Israele uja; guwa la nsembelo, ndi msanje womwe anagumula; natentha msanje, naupondereza ukhale fumbi, natentha chifanizo.


Ndi nyumba zonse zomwe za ku misanje yokhala m'mizinda ya Samariya, adazimanga mafumu a Israele kuutsa nazo mkwiyo wa Yehova, Yosiya anazichotsa, nazichitira monga mwa ntchito zonse adazichita ku Betele.


Ndipo tsopano, mukuti mudzilimbikitse kutsutsana nao ufumu wa Yehova m'dzanja la ana a Davide; ndinu aunyinji ambiri, ndi pamodzi nanu anaang'ombe agolide adawapanga Yerobowamu akhale milungu yanu.


Chitatha ichi chonse tsono, Aisraele onse opezekako anatuluka kunka kumizinda ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe mu Yuda monse, ndi mu Benjamini, mu Efuremunso, ndi mu Manase, mpaka adaziononga zonse. Pamenepo ana onse a Israele anabwerera, yense kudziko lake ndi kumizinda yao.


Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; woyenga yense anyazitsidwa ndi fanizo lake losemasema; pakuti fanizo lake loyenga lili bodza, mulibe mpweya mwa iwo.


Ndipo Mowabu adzachita manyazi chifukwa cha Kemosi, monga nyumba ya Israele inachita manyazi chifukwa cha Betele amene anamkhulupirira.


Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babiloni wagwidwa, Beli wachitidwa manyazi, Merodaki wathyokathyoka, zosema zake zachitidwa manyazi, mafano ake athyokathyoka.


Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka opalamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao.


Ndipo tsopano aonjeza kuchimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo ntchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone anaang'ombe.


Asiriya sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitidzanenanso kwa ntchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza chifundo.


Ndi mafano ake osema onse adzaphwanyika, ndi mphotho zake zonse zidzatenthedwa ndi moto, ndi mafano ake onse ndidzawapasula; pakuti anazisonkhanitsa pa mphotho ya mkazi wachiwerewere, ndipo zidzabwerera kumphotho ya mkazi wachiwerewere.


Apindulanji nalo fano losema, kuti wakulipanga analisema; fano loyenga ndi mphunzitsi wamabodza, kuti wakulipanga alikhulupirira, atapanga mafano osanena mau?


Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.


Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa