Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 5:10 - Buku Lopatulika

10 Akalonga a Yuda akunga anthu osuntha malire; ndidzawatsanulira mkwiyo wanga ngati madzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Akalonga a Yuda akunga anthu osuntha malire; ndidzawatsanulira mkwiyo wanga ngati madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Chauta akuti, “Atsogoleri a ku Yuda amachita nkhondo kuti afutuze malire. Nchifukwa chake ndidzaŵamiza ndi mkwiyo wanga ngati madzi achigumula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Atsogoleri a Yuda ali ngati anthu amene amasuntha miyala ya mʼmalire. Ndidzawakhutulira ukali wanga ngati madzi a chigumula.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 5:10
15 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake oyera mtima onse apemphere kwa Inu, pa nthawi ya kupeza Inu; indetu pakusefuka madzi aakulu sadzamfikira iye.


Muwatsanulire mkwiyo wanu, ndipo moto wa ukali wanu uwagwere.


Zinandizungulira ngati madzi tsiku lonse; zinandizinga pamodzi.


Chiyambi cha ndeu chifanana ndi kutsegulira madzi; tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.


Usasunthe chidziwitso chakale cha m'malire, chimene makolo ako anachiimika.


Akulu ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera milandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.


Monga siliva asungunuka m'kati mwa ng'anjo, momwemo inu mudzasungunuka m'kati mwake; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndakutsanulirani ukali wanga.


Katsala kamphindi, ndipo ndidzakutsanulira ukali wanga, ndi kukukwaniritsira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse.


ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.


Koma iye amene akumva, ndi kusachita, afanafana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo unagunda mtsinje, ndipo inagwa pomwepo; ndipo kugumuka kwake kwa nyumbayo kunali kwakukulu.


Musamasendeza malire a mnansi wanu, amene adawaika iwo a kale lomwe, m'cholowa chanu mudzalandirachi, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu.


Wotembereredwa iye wakusendeza malire a mnansi wake. Ndi anthu onse anene, Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa