Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 4:19 - Buku Lopatulika

19 Mphepo yamkulunga m'mapiko ake, ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Mphepo yamkulunga m'mapiko ake, ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Adzachotsedwa ngati chinthu chotengedwa ndi mphepo, ndipo adzachititsidwa manyazi chifukwa cha nsembe zao zachikunja.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Adzachotsedwa ndi kamvuluvulu ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zawo.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 4:19
13 Mawu Ofanana  

Chifukwa adzakhala ndi manyazi, chifukwa cha mitengo yathundu munaikhumba, ndipo inu mudzagwa nkhope, chifukwa cha minda imene mwaisankha.


Iwo adzabwezedwa m'mbuyo, adzakhala ndi manyazi ambiri amene akhulupirira mafano osemedwa, nati kwa mafano oyengeka, Inu ndinu milungu yathu.


Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m'dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.


Yehova atero: Taonani, ndidzaukitsira Babiloni, ndi iwo okhala mu Lebi-kamai, mphepo yoononga.


Pamene ndifuna ndidzawalanga, ndi mitundu ya anthu idzawasonkhanira pomangidwa iwo pa zolakwa zao ziwiri.


Adzachitengeranso ku Asiriya chikhale mphatso ya kwa mfumu Yarebu; Efuremu adzatenga manyazi, ndi Israele adzachita manyazi ndi uphungu wake.


Efuremu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse achulukitsa mabodza ndi chipasuko, ndipo achita pangano ndi Asiriya, natenga mafuta kunka nao ku Ejipito.


Chinkana abala mwa abale ake, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kuchokera kuchipululu; ndi gwero lake lidzaphwa, ndi kasupe wake adzauma, adzafunkha chuma cha akatundu onse ofunika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa