Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 12:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Yakobo anathawira kuthengo la Aramu, ndi Israele anagwira ntchito chifukwa cha mkazi, ndi chifukwa cha mkazi anaweta nkhosa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Yakobo anathawira kuthengo la Aramu, ndi Israele anagwira ntchito chifukwa cha mkazi, ndi chifukwa cha mkazi anaweta nkhosa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 (Yakobe adathaŵira ku dziko la Aramu. Israeleyo adagwira ntchito kumeneko kuti apeze mkazi. Ankaŵeta nkhosa kuti akwatire mkaziyo).

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Yakobo anathawira ku dziko la Aramu, Israeli anagwira ntchito kuti apeze mkazi, ndipo anaweta nkhosa kuti akwatire mkaziyo.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 12:12
9 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano mwana wanga, tamvera mau anga: tauka, nuthawire kwa Labani mlongo wanga ku Harani;


Undipatse ine akazi anga ndi ana anga chifukwa cha iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: chifukwa udziwa iwe ntchito imene ndinakugwirira iwe.


Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako aakazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.


Chinkana iwe, Israele, uchita uhule, koma asapalamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.


Giliyadi ndiwo mzinda wa ochita zoipa, wa mapazi a mwazi.


Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye Mwaramu wakuti atayike, natsika kunka ku Ejipito, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang'ono, nasandukako mtundu waukulu, wamphamvu, ndi wochuluka anthu ake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa