Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Hoseya 12:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo mwa mneneri Yehova anakweretsa Israele kuchokera mu Ejipito, ndi mwa mneneri anasungika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo mwa mneneri Yehova anakweretsa Israele kuchokera m'Ejipito, ndi mwa mneneri anasungika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Chauta adatulutsa Aisraele ku Ejipito kudzera mwa mneneri. Ndipo mwa mneneriyo adaŵasungabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Yehova anagwiritsa ntchito mneneri kuti atulutse Israeli mu Igupto; kudzera mwa mneneriyo Iye anawasamalira.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 12:13
17 Mawu Ofanana  

Tauka, nupite ku Padanaramu, kunyumba ya Betuele, atate wa amai ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana aakazi a Labani mlongo wake wa amai ako.


Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka chifukwa cha chikondi chimene anamkonda iye nacho.


Munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa, ndi dzanja la Mose ndi Aroni.


Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa.


Ndipo mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israele, unachokako, nutsata pambuyo pao; ndipo mtambo njo uja unachoka patsogolo pao, nuima pambuyo pao;


Pamene Israele anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali mu Ejipito.


Ndipo ndidzampatsa minda yake yampesa kuyambira pomwepo, ndi chigwa cha Akori chikhale khomo la chiyembekezo; ndipo adzavomereza pomwepo monga masiku a ubwana wake, ndi monga tsiku lokwera iye kutuluka m'dziko la Ejipito.


Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu.


Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, moonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose.


Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye Mwaramu wakuti atayike, natsika kunka ku Ejipito, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang'ono, nasandukako mtundu waukulu, wamphamvu, ndi wochuluka anthu ake;


Pamene Yakobo anafika ku Ejipito, ndi makolo anu anapemphera kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose ndi Aroni, amene anatulutsa makolo anu mu Ejipito, nawakhalitsa pamalo pano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa