Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hagai 2:3 - Buku Lopatulika

3 Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi mu ulemerero wake woyamba? Ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m'maso mwanu ngati chabe?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi m'ulemerero wake woyamba? Ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m'maso mwanu ngati chabe?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 “Kodi alipo ena mwa inu amene adaaona ulemerero wakale wa Nyumba iyi? Monga simukuwona kuti tsopano ulemererowo watheratu?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 ‘Kodi alipo amene watsala pakati panu amene anaona ulemerero wakale wa Nyumba iyi? Nanga tsopano ikuoneka motani kwa inu? Kodi sikuoneka ngati yopanda pake kwa inu?

Onani mutuwo Koperani




Hagai 2:3
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anati, Solomoni mwana wanga ndiye mnyamata ndi wosakhwima, ndi nyumba imene adzaimangira Yehova ikhale yaikulu yopambana, yomveka ndi ya ulemerero mwa maiko onse; ndiikonzeretu mirimo. Momwemo Davide anakonzeratu mochuluka asanamwalire.


Ndipo anathirirana mang'ombe, kulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi kuti, Pakuti ndiye wabwino, pakuti chifundo chake nchosalekeza pa Israele. Nafuula anthu onse ndi chimfuu chachikulu, pomlemekeza Yehova; popeza adamanga maziko a nyumba ya Yehova.


Koma ansembe ambiri, ndi Alevi, ndi akulu a nyumba za makolo, okalamba amene adaona nyumba yoyamba ija, pomanga maziko a nyumba iyi pamaso pao, analira ndi mau aakulu; koma ambiri anafuulitsa mokondwera.


Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu, Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu wasanduka bwinja.


Ndipo chokometsera chake chokongola anachiyesa chodzikuza nacho, napangira mafanizo olaula, ndi zonyansa zao zina; chifukwa chake ndinapatsa ichi chikhale chowadetsa.


Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m'malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa