Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hagai 1:2 - Buku Lopatulika

2 Atero Yehova wa makamu, akuti, Anthu awa anena, Nthawi siinafike, nthawi yakumanga nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Atero Yehova wa makamu, akuti, Anthu awa anena, Nthawi siinafike, nthawi yakumanga nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Anthu aŵa amanena kuti, ‘Nthaŵi siinafike yoti nkumanganso Nyumba ya Chauta.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu awa amanena kuti, ‘Nthawi sinafike yoti nʼkumanga Nyumba ya Yehova.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Hagai 1:2
14 Mawu Ofanana  

Pamenepo mfumu Yowasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndalama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba.


Pamenepo atawerenga malemba a kalata ya mfumu Arita-kisereksesi kwa Rehumu, ndi Simisai mlembi, ndi anzao, anafulumira kupita ku Yerusalemu kwa Ayuda, nawaletsa ndi dzanja lamphamvu.


Ndipo Ayuda anati, Mphamvu ya osenza akatundu yatha, ndi dothi lichuluka, motero sitidzakhoza kumanga lingali.


Waulesi ati, Pali mkango panjapo, ndidzaphedwa pamakwalalapo.


Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.


Woyang'ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.


mphindi yakupha ndi mphindi yakuchiza; mphindi yakupasula ndi mphindi yakumanga;


Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.


Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti,


Pamenepo mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,


Koma anthu adakwera nayewo anati, Sitingathe kuwakwerera anthuwo; popeza atiposa mphamvu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa