Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 7:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo zinaonongedwa zamoyo zonse zimene zinali padziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndipo zinaonongedwa padziko lapansi: anatsala Nowa yekha ndi amene anali pamodzi naye m'chingalawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo zinaonongedwa zamoyo zonse zimene zinali pa dziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndipo zinaonongedwa pa dziko lapansi: anatsala Nowa yekha ndi amene anali pamodzi naye m'chingalawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Chauta adaononga zamoyo zonse za pa dziko: anthu, nyama, zokwaŵa ndi mbalame. Nowa yekha adapulumuka pamodzi ndi onse amene anali naye m'chombomo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Chamoyo chilichonse pa dziko lapansi chinawonongedwa, kuyambira munthu, nyama, zokwawa ndi mbalame. Nowa yekha ndiye anatsala pamodzi ndi onse amene anali naye.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 7:23
21 Mawu Ofanana  

Ndine, taonani, ndipo Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi padziko lapansi, kuti chiononge zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo pansi pathambo; zinthu zonse za m'dziko lapansi zidzafa.


Ndipo anatuluka Nowa ndi ana ake, ndi mkazi wake, ndi akazi a ana ake, pamodzi naye:


Adzakupulumutsa m'masautso asanu ndi limodzi; chinkana mwa asanu ndi awiri palibe choipa chidzakukhudza.


Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.


Pambali pako padzagwa chikwi, ndi zikwi khumi padzanja lamanja lako; sichidzakuyandikiza iwe.


Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.


Ndipo amenewa adzachoka kunka ku chilango cha nthawi zonse; koma olungama kumoyo wa nthawi zonse.


Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.


imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka chingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;


ndipo sanalekerere dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula;


Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;


mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidaonongeka;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa