Genesis 6:16 - Buku Lopatulika16 Uike zenera m'chingalawacho, ulimalize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pake: khomo la chingalawa uike m'mbali mwake; nuchipange ndi nyumba yapansi, ndi yachiwiri, ndi yachitatu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Uike zenera m'chingalawacho, ulimalize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pake: khomo la chingalawa uike m'mbali mwake; nuchipange ndi nyumba yapansi, ndi yachiwiri, ndi yachitatu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Upange denga la chombocho, ndipo usiye mpata wa masentimita 50 pakati pa dengalo ndi mbali zake. Uchimange mosanjikiza, chikhale cha nyumba zitatu, ndipo m'mbali mwake mukhale chitseko. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Uchipangire denga ndi kuchimaliza ndi zenera la masentimita makumi asanu. Uyike khomo mʼmbali mwa chombocho ndi kupanga zipinda zosanjikana; chapansi, chapakati ndi chapamwamba. Onani mutuwo |