Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 50:5 - Buku Lopatulika

5 Atate wanga anandilumbiritsa ine, kuti, Taona, ndilinkufa; m'manda m'mene ndadzikonzeratu ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundiloletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabweranso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Atate wanga anandilumbiritsa ine, kuti, Taona, ndilinkufa; m'manda m'mene ndadzikonzeratu ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundiloletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabweranso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 ‘Pamene bambo wanga anali pafupi kufa, adandilumbiritsa kuti ndikamuike m'manda amene adadzikumbira m'dziko la Kanani. Motero chonde, mundilole kuti ndipite ndikaike bambo wanga, pambuyo pake ndidzabweranso.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 ‘Abambo anga anandilumbiritsa ndipo anati, ‘Ndatsala pangʼono kumwalira, ukandiyike mʼmanda amene ndinakumba ndekha mʼdziko la Kanaani.’ Tsono mundilole ndikayike abambo anga, ndipo ndikabweranso.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 50:5
19 Mawu Ofanana  

m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.


Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Taona, ndilinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako.


Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.


Atapita masiku akumlira iye, Yosefe anati kwa mbumba ya Farao, kuti, Ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, nenanitu m'makutu a Farao kuti,


Ndipo Farao anati, Pita, kaike atate wako, monga iye anakulumbiritsa iwe.


Ndipo anamuika m'manda ake adadzisemerawo m'mzinda wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundumitundu, monga mwa makonzedwe a osakaniza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri.


Pakuti ndidziwa kuti mudzandifikitsa kuimfa, ndi kunyumba yokomanamo amoyo onse.


Anakhetsa mwazi wao ngati madzi pozungulira Yerusalemu; ndipo panalibe wakuwaika.


inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsa; katungurume adzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja;


fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.


Chinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zake ndi kuchuluka, koma mtima wake osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo;


Uchitanji iwe kuno, ndimo ndani ali nawe kuno, kuti iwe wagoba manda kuno, ndi kudzigobera manda pamwamba, ndi kudzisemera mogonamo m'thanthwe.


nauika m'manda ake atsopano, osemedwa m'mwala, nakunkhunizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo.


pakuti ndidzafa m'dziko muno, osaoloka Yordani; koma inu mudzaoloka, ndi kulandira dziko ili lokoma likhale lanulanu.


Pamenepo Saulo ananena ndi Yonatani, Undiuze chimene unachita. Ndipo Yonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo inali m'dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa