Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 49:31 - Buku Lopatulika

31 pamenepo anaika Abrahamu ndi Sara mkazi wake; pamenepo anaika Isaki ndi Rebeka mkazi wake: pamenepo ndinaika Leya:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 pamenepo anaika Abrahamu ndi Sara mkazi wake; pamenepo anaika Isaki ndi Rebeka mkazi wake: pamenepo ndinaika Leya:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Kumeneko ndiko kumene adaika Abrahamu pamodzi ndi Sara mkazi wake. Isaki pamodzi ndi mkazi wake Rebeka, adaŵaikanso komweko, ndipo Leya ndidamuika komwekonso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Kumeneko kunayikidwa Abrahamu ndi mkazi wake Sara, Isake ndi mkazi wake Rebeka ndipo ndinayikakonso Leya.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 49:31
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anauka pa wakufa wake, nanena kwa ana a Hiti, nati,


munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Hiti. Pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wake.


Ndipo ana ake Isaki ndi Ismaele anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efuroni mwana wake wa Zohari Muhiti, umene uli patsogolo pa Mamure;


Ndipo Labani anali ndi ana aakazi awiri, dzina la wamkulu ndi Leya, dzina la wamng'ono ndi Rakele.


Ndipo Isaki anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ake aamuna anamuika iye.


koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kutuluka m'dziko la Ejipito, ukandiike ine m'manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzachita monga mwanena.


munda ndi phanga lili m'menemo, zinagulidwa kwa ana a Hiti


chifukwa kuti ana ake aamuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure.


ndipo anawanyamula kupita nao ku Sekemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Hamori mu Sekemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa