Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 49:22 - Buku Lopatulika

22 Yosefe ndi nthambi yobala, nthambi yobala pambali pa kasupe; nthambi zake ziyangayanga palinga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Yosefe ndi nthambi yobala, nthambi yobala pambali pa kasupe; nthambi zake ziyangayanga palinga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 “Yosefe ali ngati nthambi yobala zipatso, nthambi yobala zipatso pafupi ndi kasupe, nthambi yotambasuka pa khoma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 “Yosefe ali ngati mtengo wobereka zipatso, mtengo wobereka zipatso pafupi ndi kasupe, nthambi zake zimayanga pa chipupa cha mwala.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 49:22
19 Mawu Ofanana  

Ndipo dzina la wachiwiri anamutcha Efuremu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.


ndi ana aamuna a Yosefe, amene anambadwira iye mu Ejipito ndiwo anthu awiri; anthu onse a mbumba ya Yakobo, amene analowa mu Ejipito anali makumi asanu ndi awiri.


Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake aamuna awiri, Manase ndi Efuremu, apite naye.


Ndipo anadalitsa Yosefe, nati, Mulungu, pamaso pake anayenda makolo anga Abrahamu ndi Isaki, Mulungu amene anandidyetsa ine nthawi zonse za moyo wanga kufikira lero,


mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati padziko lapansi.


Tsopano ana ako aamuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga.


Eni uta anavutitsa iye kwambiri, namponyera iye, namzunza.


Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake.


Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.


Mthunzi wake unaphimba mapiri, ndi nthambi zake zikunga mikungudza ya Mulungu.


Ndipo unali nazo ndodo zolimba zikhale ndodo zachifumu, za ochita ufumu, ndi msinkhu wao unakula kufikira kumitambo, ndipo zinaoneka m'kusomphoka kwao pakati pa nthambi zake zambiri.


Chinkana abala mwa abale ake, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kuchokera kuchipululu; ndi gwero lake lidzaphwa, ndi kasupe wake adzauma, adzafunkha chuma cha akatundu onse ofunika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa