Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 49:16 - Buku Lopatulika

16 Dani adzaweruza anthu ake, monga limodzi la mafuko a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Dani adzaweruza anthu ake, monga limodzi la mafuko a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 “Dani adzalamulira anthu ake. Anthuwo adzalingana ndi mafuko ena a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 “Dani adzaweruza mwachilungamo anthu ake monga limodzi mwa mafuko a anthu a mu Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 49:16
10 Mawu Ofanana  

Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; chifukwa chake anamutcha dzina lake Dani.


Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino, ndi dziko kuti linali lokondweretsa; ndipo anaweramitsa phewa lake kuti anyamule, nakhala kapolo wakugwira ntchito ya msonkho.


Dani adzakhala njoka m'khwalala, songo panjira, imene iluma zitendene za kavalo, kuti womkwera wake agwe chambuyo.


Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Ahiyezere mwana wa Amisadai.


Ndi za Dani anati, Dani ndiye mwana wa mkango, wakutumpha motuluka mu Basani.


Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lake ndiye Manowa; ndi mkazi wake analibe mwana, sanabale.


Ndipo Samisoni anaweruza Israele m'masiku a Afilisti zaka makumi awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa