Genesis 47:26 - Buku Lopatulika26 Ndipo Yosefe analamulira lamulo la padziko la Ejipito kufikira lero, kuti Farao alandire limodzi la mwa magawo asanu; koma dziko la ansembe lokha silinakhale la Farao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201426 Ndipo Yosefe analamulira lamulo la pa dziko la Ejipito kufikira lero, kuti Farao alandire limodzi la mwa magawo asanu; koma dziko la ansembe lokha silinakhala la Farao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa26 Motero Yosefe adapanga lamulo m'dziko lonse la Ejipito, kuti chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse pa zokolola chidzakhala cha Farao. Lamulo limeneli lilipobe mpaka lero lino. Koma maiko a ansembe okha sadaŵatenge kuti akhale a Farao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero26 Choncho Yosefe anakhazikitsa lamulo limene lilipobe mpaka lero mʼdziko lonse la Igupto kuti limodzi la magawo asanu a zokolola ndi la Farao. Ndi minda ya ansembe yokha imene sinatengedwe kukhala ya Farao. Onani mutuwo |