Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 47:18 - Buku Lopatulika

18 Chitatha chaka chimenecho, anadza kwa iye chaka chachiwiri, nati kwa iye, Sitibisira mbuyathu kuti ndalama zathu zonse zatha; ndipo zoweta za ng'ombe nza mbuyathu: palibe kanthu kotsala pamaso pa mbuyathu, koma matupi athu ndi maiko athu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Chitatha chaka chimenecho, anadza kwa iye chaka chachiwiri, nati kwa iye, Sitibisira mbuyathu kuti ndalama zathu zonse zatha; ndipo zoweta za ng'ombe nza mbuyathu: palibe kanthu kotsala pamaso pa mbuyathu, koma matupi athu ndi maiko athu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Chitatha chaka chimenecho, anthuwo adapitanso kwa Yosefe namuuza kuti, “Bwana, ife sitingakubisireni kuti ndalama zathu pamodzi ndi zoŵeta zathu zomwe, zatithera. Palibe chilichonse chotsala choti tingathe kukupatsani, tingodzipereka ifeyo ndi minda yathuyi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Chitatha chaka chimenecho, anthu anapitanso kwa Yosefe chaka chinacho nati, “Ife sitingakubisireni mbuye wathu kuti ndalama zathu zatithera ndipo ziweto zathu zili ndi inu, palibenso choti nʼkukupatsani mbuye wathu kupatula matupi athu ndi dziko lathu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 47:18
4 Mawu Ofanana  

Ndipo anadza nazo ng'ombe zao kwa Yosefe, ndipo Yosefe anapatsa iwo chakudya chosinthana ndi akavalo, ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi abulu; ndipo anawadyetsa iwo ndi chakudya chosinthana ndi zoweta zao zonse chaka chimenecho.


tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? Mutigule ife ndi dziko lathu ndi chakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja.


Ndipo popita mfumu ya Israele alikuyenda palinga, mkazi anamfuulira, nati, Ndithandizeni, mbuye wanga mfumu.


Mbuyanga mfumu, anthu awa anachita zoipa m'zonse anachitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo chifukwa cha njala; pakuti mulibe chakudya china m'mzindamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa