Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 47:19 - Buku Lopatulika

19 tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? Mutigule ife ndi dziko lathu ndi chakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? Mutigule ife ndi dziko lathu ndi chakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Musatilekerere kuti tife m'dziko mwathu, inu mukuwona. Mutipatseko chakudya, ndipo tidzigulitsa ifeyo ndi minda yathu yomwe. Tidzakhala akapolo a Farao, iye adzatenga minda yathu kuti ikhale yake. Mutipatseko mbeu kuti tisafe ndi njala, kutinso minda yathu isakhale masala.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Tiferenji ife ndi dziko lathu inu mukuona? Mutipatse chakudya ndipo tidzigulitsa ife ndi minda yathu yomwe. Ife tidzakhala akapolo a Farao. Tipatseni mbewuzo kuti tikhale ndi moyo tisafe ndipo dziko lisachite bwinja.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 47:19
11 Mawu Ofanana  

Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala.


Ndipo zitatha ndalama zonse m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, Aejipito onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife chakudya; tiferenji pamaso panu? Zatsirizika ndalama.


Chitatha chaka chimenecho, anadza kwa iye chaka chachiwiri, nati kwa iye, Sitibisira mbuyathu kuti ndalama zathu zonse zatha; ndipo zoweta za ng'ombe nza mbuyathu: palibe kanthu kotsala pamaso pa mbuyathu, koma matupi athu ndi maiko athu;


Ndipo Yosefe anamgulira Farao dziko lonse la Ejipito, chifukwa Aejipito anagulitsa yense munda wake, chifukwa njala inakula pa iwo; ndipo dziko linakhala la Farao.


Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.


Anthu ake onse ausa moyo nafunafuna mkate; ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao; taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa.


Tinagwira mwendo Ejipito ndi Asiriya kuti tikhute zakudya.


Timalowa m'zoopsa potenga zakudya zathu, chifukwa cha lupanga la m'chipululu.


Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa