Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 47:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo anadza nazo ng'ombe zao kwa Yosefe, ndipo Yosefe anapatsa iwo chakudya chosinthana ndi akavalo, ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi abulu; ndipo anawadyetsa iwo ndi chakudya chosinthana ndi zoweta zao zonse chaka chimenecho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo anadza nazo ng'ombe zao kwa Yosefe, ndipo Yosefe anapatsa iwo chakudya chosinthana ndi akavalo, ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi abulu; ndipo anawadyetsa iwo ndi chakudya chosinthana ndi zoweta zao zonse chaka chimenecho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Motero adabwera ndi zoŵeta zao kwa Yosefe, nasinthitsa ndi chakudya zoŵeta zaozo, monga akavalo, nkhosa ndi mbuzi, ng'ombe ndi abulu. Chaka chimenecho Yosefe adaŵapatsa chakudya anthuwo mosinthana ndi zoŵeta zaozo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Choncho anthu anabwera ndi ziweto zawo monga akavalo, nkhosa, mbuzi, ngʼombe ndi abulu ndipo Yosefe anawapatsa zakudya.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 47:17
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe anati, Mundipatse ng'ombe zanu: ndipo ndidzakupatsani inu mtengo wa ng'ombe zanu ngati ndalama zatsirizika.


Chitatha chaka chimenecho, anadza kwa iye chaka chachiwiri, nati kwa iye, Sitibisira mbuyathu kuti ndalama zathu zonse zatha; ndipo zoweta za ng'ombe nza mbuyathu: palibe kanthu kotsala pamaso pa mbuyathu, koma matupi athu ndi maiko athu;


Ndipo akavalo a Solomoni anachokera ku Ejipito; anthu a malonda a mfumu anawagula magulumagulu, gulu lililonse mtengo wake.


Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.


taona, dzanja la Yehova lidzakhala pa zoweta zako za kubusa, pa akavalo, pa abulu, pa ngamira, pa ng'ombe, ndi pa zoweta zazing'ono ndi kalira woopsa.


Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Ejipito kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magaleta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang'ana Woyera wa Israele, ngakhale kumfuna Yehova!


Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa