Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 45:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo anamfotokozera iye mau onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anaona magaleta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wao unatsitsimuka;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo anamfotokozera iye mau onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anaona magaleta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wao unatsitsimuka;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Komabe iwo atamuuza zonse zimene Yosefe adaaŵauza, ndipo iye ataona ngolo zimene Yosefe adaatumiza kuti iye akwerepo popita ku Ejipito, Yakobe adayamba kutsitsimuka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Komabe atamufotokozera zonse zimene Yosefe anawawuza ndipo ataona ngolo zimene Yosefe anatumiza kuti adzakweremo popita ku Igupto, mtima wa Yakobo, abambo awo unatsitsimuka.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 45:27
8 Mawu Ofanana  

Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m'dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu.


ndipo Israele anati, Chakwana; Yosefe mwana wanga akali ndi moyo; ndidzamuka ndikamuone iye ndisanafe.


Kodi simudzatipatsanso moyo, kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?


Monga madzi ozizira kwa munthu wotopa, momwemo mau abwino akuchokera kudziko lakutali.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake.


Pamenepo Mulungu anang'amba pokumbika paja pa Lehi, natulukamo madzi; namwa iye, nubwera moyo wake, natsitsimuka iye; chifukwa chake anawatcha dzina lake, Kasupe wa wofuula, ndiwo mu Lehi mpaka lero lino.


nampatsanso chigamphu cha nchinchi ya nkhuyu ndi nchinchi ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wake unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya chakudya, osamwa madzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa