Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 45:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m'dziko lonse la Ejipito. Pamenepo mtima wake unakomoka, pakuti sanawakhulupirire iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m'dziko lonse la Ejipito. Pamenepo mtima wake unakomoka, pakuti sanawakhulupirire iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Atafika, adauza bambo wao kuti, “Yosefe ujatu ali moyo! Ndiye wolamulira Ejipito yense!” Yakobe adachita ngati wakomoka, pakuti sadakhulupirire zonena zaozo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Iwo anawuza abambo awo kuti, “Yosefe akanali ndi moyo! Ndiponsotu, ndiye akulamulira dziko la Igupto.” Yakobo anangoti kakasi osankhulupirira.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 45:26
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenga malaya ake a Yosefe, napha tonde, naviika malaya m'mwazi wake:


Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.


Ndipo anadza kwa Yakobo atate wao ku dziko la Kanani, namfotokozera iye zonse zinaonekera kwa iwo;


Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzachotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera.


Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.


wina anatuluka kwa ine ndipo ndinati, Zoonatu, wakadzulidwa; ndipo sindidzamuonanso iye;


Ndipo anakwera kutuluka mu Ejipito, nafika ku dziko la Kanani kwa Yakobo atate wao.


Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Sindinaganizira kuti ndiona nkhope yako: ndipo, taona, Mulungu wandionetsa ine mbeu zako zomwe.


Ndinawaseka akapanda kulimbika mtima; ndipo sanagwetse kusangalala kwa nkhope yanga.


Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye, koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga.


Anamuika akhale woyang'anira nyumba yake, ndi woweruza wa pa zake zonse:


Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, tinakhala ngati anthu akulota.


Pokomoka moyo wanga m'kati mwanga ndinakumbukira Yehova; ndi pemphero langa linafikira Inu mu Kachisi wanu wopatulika.


Ndipo mau awa anaoneka pamaso pao ngati nkhani zachabe, ndipo sanamvere akaziwo.


nanena, Ambuye anauka ndithu, naonekera kwa Simoni.


Koma pokhala iwo chikhalire osakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa