Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 45:23 - Buku Lopatulika

23 Kwa atate wake anatumiza zotere: abulu khumi osenza zinthu zabwino za mu Ejipito, ndi abulu aakazi khumi osenza tirigu, ndi chakudya, ndi phoso la atate la panjira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Kwa atate wake anatumiza zotere: abulu khumi osenza zinthu zabwino za m'Ejipito, ndi abulu akazi khumi osenza tirigu, ndi chakudya, ndi phoso la atate la panjira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Bambo wake adamtumizira abulu khumi osenza zipatso zokoma za ku Ejipito, ndi abulu khumi osenza tirigu, buledi ndi zakudya zina za bambo wake zapaulendo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Ndipo abambo ake anawatumizira izi: abulu khumi osenza zinthu zabwino kwambiri za ku Igupto, ndi abulu aakazi khumi osenza tirigu, buledi ndi zakudya zina za pa ulendo wake.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 45:23
5 Mawu Ofanana  

Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.


Ndipo Israele atate wao anati kwa iwo, Ngati chomwecho tsopano chitani ichi: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta amankhwala pang'ono, ndi uchi pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;


Onse anawapatsa yense zovala zopindula; koma Benjamini anampatsa masekeli a siliva mazana atatu ndi zovala zopindula zisanu.


Ndipo anamukitsa abale ake, ndipo anachoka; ndipo anati kwa iwo, Musakangane panjira.


nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m'chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa