Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 45:20 - Buku Lopatulika

20 Musasamalire chuma chanu; popeza zabwino za dziko lonse la Ejipito ndi zanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Musasamalire chuma chanu; popeza zabwino za dziko lonse la Ejipito ndi zanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Asakade nkhaŵa kuti asiya katundu wao kumeneko, chifukwa dziko lokoma lachonde la ku Ejipito kuno lidzakhala lao.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Musadandaule zosiya katundu komweko chifukwa dziko lachonde la kuno ku Igupto lidzakhala lanu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 45:20
23 Mawu Ofanana  

Ndipo Abimeleki anati, Taona dziko langa lili pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko.


katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Ejipito, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli.


Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m'dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu.


Ndipo ana a Israele anachita chotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magaleta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira.


dziko la Ejipito lili pamaso pako: uwakhazike atate wako ndi abale ako pa dera lokometsetsa la dziko; akhale m'dziko la Goseni; ndipo ngati udziwa anthu anzeru a mwa iwo, uwaike iwo ayang'anire ng'ombe zanga.


Chifukwa chake tsono, musamapereka ana anu akazi kwa ana ao aamuna, kapena kutengera ana anu aamuna ana ao akazi, kapena kufuna mtendere wao ndi kukoma kwao nthawi yonse, kuti mukhale olimba, ndi kudya zokoma za m'dziko, ndi kulisiyira ana anu cholowa cha kunthawi yonse.


Munthu akaikiza ndalama kapena chuma kwa mnansi wake, ndipo zibedwa m'nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe chowirikiza.


Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko,


Mauta ao adzatha anyamata; ndipo sadzachitira chisoni chipatso cha mimba; diso lao silidzaleka ana.


Koma diso langa lidawaleka osawaononga, sindinawathe onse m'chipululu.


Ndipo diso langa silidzakulekerera, sindidzachita chifundo, koma ndidzakubwezera njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo diso langa silidzalekerera, wosachita chifundo Ine, ndidzakubwezera monga mwa njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakukantha.


Nati kwa enawo, ndilikumva ine, Pitani pakati pa mzinda kumtsata iye, ndi kukantha; maso anu asalekerere, musachite chifundo;


iye ali pamwamba pa tsindwi, asatsikire kunyamula za m'nyumba mwake;


Tsikulo iye amene adzakhala pamwamba pa tsindwi, ndi akatundu ake m'nyumba, asatsike kuwatenga; ndipo iye amene ali m'munda modzimodzi asabwere ku zake za m'mbuyo.


Diso lanu lisamchitire chifundo, koma muchotse mwazi wosachimwa mu Israele, kuti chikukomereni.


Ndipo diso lanu lisachite chifundo, moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi.


Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawachitire chifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakuchitirani msampha.


Israele wachimwa, nalakwiranso chipangano changa, ndinawalamuliracho; natengakonso choperekedwacho; anabanso, nanyenganso, nachiika pakati pa akatundu ao.


Chifukwa chake anaonjeza kufunsa Yehova, Watsala wina kodi woyenera kubwera kuno? Ndipo Yehova anati, Onani, alikubisala pakati pa akatundu.


Ndipo Davide anati kwa anthu ake, Munthu yense wa inu amangirire lupanga lake. Namangirira munthu yense lupanga lake; ndi Davide yemwe anamangirira lupanga lake; ndipo anakwera kumtsata Davide monga anthu mazana anai, koma mazana awiri anadika akatundu.


Ndipo ndani adzavomerezana nanu mlandu uwu? Pakuti monga gawo lake la iye wakumuka kunkhondoko, momwemo lidzakhala gawo lake la iye wakukhala ndi akatundu, adzagawana chimodzimodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa