Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 45:18 - Buku Lopatulika

18 katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Ejipito, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Ejipito, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Tsono kumeneko akatenge bambo wao ndi mabanja ao, ndipo adzabwere kwa ine kuno. Ndidzaŵapatsa dziko lachonde ku Ejipito kuno, ndipo azidzadya za m'dziko lino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Mukabwere nawo abambo anu ndi mabanja anu kuno, ndipo ine ndidzakupatsani dera lachonde kwambiri mʼdziko la Igupto. Mudzadya zokoma za mʼdzikoli.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 45:18
11 Mawu Ofanana  

Mulungu akupatse iwe mame a kumwamba, ndi zonenepa za dziko lapansi, ndi tirigu wambiri ndi vinyo.


Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Nena ndi abale ako, Chitani ichi; senzetsani nyama zanu, ndi kupita kunka ku dziko la Kanani;


Mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng'ombe chiyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m'dziko la Goseni; chifukwa abusa onse anyansira Aejipito.


dziko la Ejipito lili pamaso pako: uwakhazike atate wako ndi abale ako pa dera lokometsetsa la dziko; akhale m'dziko la Goseni; ndipo ngati udziwa anthu anzeru a mwa iwo, uwaike iwo ayang'anire ng'ombe zanga.


Ndiye amene akhalitsa malire anu mumtendere; akukhutitsani ndi tirigu wakucha bwino.


Akadawadyetsa naye tirigu wokometsetsa, ndikadakukhutitsanso ndi uchi wa m'thanthwe.


Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efuremu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'chigwa cha nthaka yabwino.


ndi duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu pa chigwa cha nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kucha malimwe asanafike; poiona wakupenya imeneyo, amaidya ili m'dzanja lake.


Mafuta onse okometsetsa, ndi vinyo watsopano, ndi tirigu yense wokometsetsa. Zipatso zao zoyamba zimene aziperekako kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe.


Mupereke nsembe zokweza zonse za Yehova kuzitenga ku mphatso zanu zonse, kusankhako zokometsetsa ndizo zopatulika zake.


mafuta a mkaka wang'ombe, ndi mkaka wankhosa, ndi mafuta a anaankhosa, ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basani, ndi atonde, ndi impso zonenepa zatirigu; ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa