Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 45:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse mu Ejipito, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse m'Ejipito, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Muuzeni bambo wanga kuti ndili pa ulemerero waukulu ku Ejipito kuno. Mukamuuzenso bambo wanga zonse zimene mwaonazi ndipo fulumirani, mubwere naye kuno.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Mukawawuze abambo anga kuti ndili pa ulemerero ku dziko la Igupto kuno ndi zonse zimene mwaziona. Tsopano fulumirani kuti mukabwere nawo kuno abambo anga.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 45:13
5 Mawu Ofanana  

Taonani, maso anu aona, ndi maso a mphwanga Benjamini, kuti ndi m'kamwa mwanga ndilikulankhula ndi inu.


Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.


Ndipo Yosefe anatumiza, naitana Yakobo atate wake, ndi a banja lake lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu.


Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa