Genesis 44:18 - Buku Lopatulika18 Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngati Farao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngati Farao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Pamenepo Yuda adasendera kwa Yosefe, nati “Pepani bwana, loleni ine mtumiki wanu kuti ndilankhule nanu. Musati mukwiye nane bwana, inu muli ngati Farao yemwe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Ndipo Yuda anamuyandikira iye nati, “Chonde mbuye wanga mulole kapolo wanune ndinene mawu pangʼono kwa mbuye wanga. Musandipsere mtima, kapolo wanune, popeza inu muli ngati Farao yemwe. Onani mutuwo |
Mukavomereza tsono, pakumva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, chabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu yemwe adzakulanditsani m'manja mwanga ndani?