Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 44:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo iye anati, Ngati kutheka kuti ndichite chotero! Munthu amene anampeza nacho m'dzanja lake adzakhala kapolo wanga: koma inu, kazipitani ndi mtendere kwa atate wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo iye anati, Ngati kutheka kuti ndichite chotero! Munthu amene anampeza nacho m'dzanja lake adzakhala kapolo wanga: koma inu, kazipitani ndi mtendere kwa atate wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Koma Yosefe adati, “Iyai! Ine sindingathe kuchita zotero. Yekhayo amene wapezeka ndi chikho, ndiye adzakhala kapolo wanga. Enanu mungathe kumabwerera kwanu kwa bambo wanu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Koma Yosefe anati, “Sindingachite choncho ayi! Yekhayo amene wapezeka ndi chikhocho ndi amene akhale kapolo wanga. Ena nonsenu, bwererani kwa abambo anu mu mtendere.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 44:17
10 Mawu Ofanana  

Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?


kuti usatichitire ife zoipa, pakuti sitidakhudze iwe, sitidakuchitire kanthu koma kabwino ndiko, ndipo takulola umuke ndi mtendere; ndiwe tsopano wodalitsidwa ndi Yehova.


Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lachitatu, Chitani ichi, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu;


Ndipo iye anati, Tsononso chikhale monga mwa mau anu: iye amene ampeza nacho adzakhala kapolo wanga; ndipo inu mudzakhala opanda chifukwa.


Ndipo Yuda anati, Kodi tidzati bwanji kwa mbuyanga? Kodi tidzanenanji? Kapena tidzawiringula ife bwanji? Mulungu wapeza mphulupulu ya akapolo anu; taonani, tili akapolo a mbuyanga, ife ndi iye amene anampeza nacho chikho m'dzanja lake.


Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngati Farao.


Mulungu wa Israele anati, Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine; kudzakhala woweruza anthu molungama; woweruza m'kuopa Mulungu.


Pakuona nyengo yake ndidzaweruza molunjika.


Wokometsa mlandu wa wamphulupulu, ndi wotsutsa wolungama, onse awiriwa amnyansa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa