Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 43:32 - Buku Lopatulika

32 Ndipo anamuikira iye chake pa yekha, ndi iwo chao pa okha, ndi Aejipito akudya naye chao pa okha; chifukwa Aejipito sanathei kudya chakudya pamodzi ndi Ahebri: chifukwa kuchita chomwecho nkunyansira Aejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndipo anamuikira iye chake pa yekha, ndi iwo chao pa okha, ndi Aejipito akudya naye chao pa okha; chifukwa Aejipito sanathei kudya chakudya pamodzi ndi Ahebri: chifukwa kuchita chomwecho nkunyansira Aejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Yosefe ankadyera payekha, abale akewo ankadyera pa tebulo lina. Aejipito amene anali naye m'nyumba nawonso ankadyera paokha, chifukwa iwo ankanyansidwa kudyera pamodzi ndi Ahebri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Anamupatsira Yosefe chakudya payekha, abale ake aja pawokha, ndiponso Aigupto amene ankadya pamodzi ndi iye nawonso pawokha. Izi zinali choncho chifukwa Aigupto ankanyansidwa kudya pamodzi ndi Ahebri.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 43:32
4 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse.


Ndipo pamene Yosefe anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wake, Lowa nao anthuwo m'nyumba, kaphere iwo, kakonzere, chifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno.


Mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng'ombe chiyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m'dziko la Goseni; chifukwa abusa onse anyansira Aejipito.


Koma Mose anati, Sikuyenera kutero; pakuti tidzamphera Yehova Mulungu wathu chonyansa cha Aejipito; taonani, ngati tikamphera nsembe chonyansa cha Aejipito pamaso pao sadzatiponya miyala kodi?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa