Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 43:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo pamene Yosefe anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wake, Lowa nao anthuwo m'nyumba, kaphere iwo, kakonzere, chifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo pamene Yosefe anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wake, Lowa nao anthuwo m'nyumba, kaphere iwo, kakonzere, chifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Yosefe ataona Benjamini, adauza wantchito woyang'anira zonse panyumba pake kuti, “Anthu aŵa aloŵetse m'nyumba. Ndipo uphe nyama ndi kuiphika bwino, chifukwa anthu ameneŵa adya ndi ine masana ano.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Yosefe ataona Benjamini ali pamodzi ndi abale ake, anati kwa wantchito wa mʼnyumba mwake, “Atengereni anthu awa ku nyumba kwanga, ndipo uphe nyama ndi kukonza bwino chakudya popeza amenewa adya ndi ine masana ano.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 43:16
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anati, Ambuye Mulungu, mudzandipatsa ine chiyani popeza ndine wopanda mwana, ndi amene adzakhala mwini nyumba yanga ndiye Eliyezere wa ku Damasiko?


Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero aakulu tsiku lomwe analetsedwa Isaki kuyamwa.


Ndipo anakonzera iwo madyerero, ndipo anadya namwa.


Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse.


Munthuyo anachita monga anamuuza Yosefe, ndipo munthuyo analowa nao anthuwo m'nyumba ya Yosefe.


Ndipo anayandikira kwa tsanyumba wa Yosefe, ndipo ananena ndi iye pa khomo la nyumba, nati,


Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wake kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi chakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lake.


Atatuluka m'mzinda asanamuke patali, Yosefe anati kwa tsanyumba wake, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Chifukwa chanji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino?


yaphera nyama yake, nisakaniza vinyo wake, nilongosolanso pa gome lake.


Kodi ndidzatenga mkate wanga, ndi madzi anga, ndi nyama imene ndinaphera osenga nkhosa anga, ndi kuzipatsa anthu amene sindidziwa kumene afumira?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa