Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 43:15 - Buku Lopatulika

15 Amunawo ndipo anatenga mphatso natenga ndalama zowirikiza m'manja mwao, ndi Benjamini; ndipo ananyamuka ndi kutsikira ku Ejipito, naima pamaso pa Yosefe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Amunawo ndipo anatenga mphatso natenga ndalama zowirikiza m'manja mwao, ndi Benjamini; ndipo ananyamuka ndi kutsikira ku Ejipito, naima pamaso pa Yosefe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Motero abale onse aja adatenga mphatso zija, ndipo adatenganso ndalama moŵirikiza, namtenganso Benjamini. Tsono adakonzeka, nanyamuka ulendo kupita ku Ejipito. Kumeneko adakaonekera pamaso pa Yosefe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Choncho abale aja anatenga mphatso, ndalama zokwanira ndi Benjamininso. Iwo anafulumira kupita ku Igupto ndipo anakaonekera kwa Yosefe.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 43:15
6 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lake; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa.


Ndipo Israele atate wao anati kwa iwo, Ngati chomwecho tsopano chitani ichi: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta amankhwala pang'ono, ndi uchi pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;


ndipo panali pamene ife tinafika pachigono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lake, ndalama zathu mkulemera kwake; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu.


Ndipo anakonzeratu mphatso asanafike Yosefe usana; chifukwa anamva kuti adzadya chakudya pamenepo.


Ndipo Zikiri munthu wamphamvu wa Efuremu anapha Maaseiya mwana wa mfumu, ndi Azirikamu woyang'anira nyumba, ndi Elikana wotsatana ndi mfumu.


Ambiri adzapembedza waufulu; ndipo yense ndi bwenzi la munthu wopatsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa