Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 42:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lake kuti adyetse bulu wake pachigono, anapeza ndalama zake; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lake kuti adyetse bulu wake pachigono, anapeza ndalama zake; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Atafika pa chigono, mmodzi mwa iwo adamasula thumba lake kuti atengeko chakudya chodyetsa bulu wake. Atamasula, adangoona kuti pakamwa pa thumbalo pali ndalama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Atafika pamalo pena poti agone, mmodzi mwa iwo anatsekula thumba lake kuti atapemo chakudya cha bulu wake. Atangomasula anaona kuti ndalama zake zili pakamwa pa thumba.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 42:27
9 Mawu Ofanana  

Natinso kwa iye, Tili nao udzu ndi zakudya zambiri ndi malo ogona.


Ndipo anasenzetsa abulu ao tirigu wao nachokapo.


Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lake; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa.


Anthuwo ndipo anaopa, chifukwa analowezedwa m'nyumba ya Yosefe; nati, Chifukwa cha ndalama zija zinabwezedwa m'matumba athu nthawi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti aone chifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi abulu athu.


Ndipo anafulumira natsitsa pansi yense thumba lake, namasula yense thumba lake.


Ndipo kunali panjira, kuchigono, Yehova anakomana naye, nafuna kumupha.


nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira.


Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m'nsalu, namgoneka modyera ng'ombe, chifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa