Genesis 42:22 - Buku Lopatulika22 Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanene kwa inu kuti, Musachimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? Chifukwa chakenso, taonani mwazi wake ufunidwa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanena kwa inu kuti, Musachimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? Chifukwa chakenso, taonani mwazi wake ufunidwa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Apo Rubeni adati, “Ine paja ndinkakuuzani kuti mnyamatuyu musamchite kanthu, inu osandimvera. Mwaonatu, tsopano tikulandira malipiro a imfa yake ija.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Rubeni anayankha, “Kodi sindinakuwuzeni kuti musamuchite kanthu mnyamata uja? Koma inu simunamvere! Tsopano tikulandira malipiro a magazi ake.” Onani mutuwo |
Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.