Genesis 42:21 - Buku Lopatulika21 Ndipo iwo anati wina ndi mnzake, Tachimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kuvutidwa kwa mtima wake, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201421 Ndipo iwo anati wina ndi mnzake, Tachimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kuvutidwa kwa mtima wake, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa21 Ndipo adayamba kuuzana kuti, “Ndithu, ife tidalakwa pamene mng'ono wathu ankatipempha kuti timchitire chifundo, koma ife osamumvera konse chifundo. Nchifukwa chake tili m'mavuto tsopano lino.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero21 Iwo anati kwa wina ndi mnzake, “Ndithu ife tinalakwira mʼbale wathu uja popeza kuti ngakhale tinaona kuvutika kwake ndi kumva kulira kwake pamene ankatidandaulira kuti timuchitire chifundo, koma ife sitinamvere. Nʼchifukwa chake masautso awa atigwera.” Onani mutuwo |