Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 41:32 - Buku Lopatulika

32 Ndipo lotolo linabwerezedwa kawiri kwa Farao, chifukwa chinthu chili chokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kuchichita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndipo lotolo linabwezedwa kawiri kwa Farao, chifukwa chinthu chili chokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kuchichita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Poti inu Farao mwalota kaŵiri maloto okhaokhaŵa, zikuwonetsa kuti Mulungu ndiye amene wakonza zimenezi, ndipo azichitadi posachedwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Popeza kuti malotowa aperekedwa kwa inu Mfumu kawiri, ndiye kuti Mulungu watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi posachedwapa.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 41:32
18 Mawu Ofanana  

pakuti taonani, ndinalinkumanga mitolo m'munda, ndipo taonani, mtolo wanga unauka nuima chilili! Ndipo taonani, mitolo yanu inadza niuzinga kwete, niuweramira mtolo wanga.


Ndipo analotanso loto lina, nafotokozera abale ake, nati, Taonani, ndalotanso loto lina: ndipo taonani, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zinandiweramira ine.


Ndipo Yosefe anati kwa Farao, Loto la Farao lili limodzi: chimene Mulungu ati achite wam'masulira Farao.


Ichi ndi chinthu chimene ndinena kwa Farao: chimene Mulungu ati achite wasonyeza kwa Farao.


ndipo zochuluka sizidzazindikirika chifukwa cha njala ikudza m'mbuyoyo, pakuti idzavuta.


Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde chifukwa cha mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wakewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wa sulufure.


Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m'phiri popanda manja, ndi kuti udapera chitsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golide; Mulungu wamkulu wadziwitsa mfumu chidzachitika m'tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwake kwakhazikika.


Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?


Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ai.


Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi:


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


koma kukhala kudzanja langa lamanja, kapena lamanzere sikuli kwanga kupatsa; koma kuli kwa iwo amene adawakonzeratu.


koma monga kulembedwa, Zimene diso silinazione, ndi khutu silinazimve, nisizinalowe mu mtima wa munthu, zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.


Nthawi yachitatu iyi ndilinkudza kwa inu. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika.


Ndipo anamasulidwa angelo anai, okonzeka kufikira ora ndi tsiku ndi mwezi ndi chaka, kuti akaphe limodzi la magawo atatu a anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa