Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 39:14 - Buku Lopatulika

14 anaitana aamuna a m'nyumba yake, nanena ndi iwo kuti, Taonani, walowetsa kwa ife Muhebri kuti atiseke ife, analowa kwa ine kugona ndi ine, ndipo ndinafuula ndi mau aakulu:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 anaitana amuna a m'nyumba yake, nanena ndi iwo kuti, Taonani, walowetsa kwa ife Muhebri kuti atiseke ife, analowa kwa ine kugona ndi ine, ndipo ndinafuula ndi mau akulu:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 adaitana antchito am'nyumbamo, naŵauza kuti, “Mwaziwona izi? Mwamuna wanga adabwera ndi Muhebri uyu m'nyumba muno kudzatipunza ife. Iye anakaloŵa kuchipinda kwanga nandinyenga kuti ndigone naye. Koma ine ndinakuŵa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 iye anayitana antchito ake a mʼnyumba nati, “Taonani mwamuna wanga anabwera ndi Mhebri uyu mʼnyumba muno kuti adzagone nane. Iyeyu analowa ku chipinda kwanga kuti adzagone nane ndipo ine ndinakuwa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 39:14
21 Mawu Ofanana  

Ndiponso kwa Semu atate wa ana onse a Eberi, mkulu wa Yafeti, kwa iye kunabadwa ana.


Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.


Ndipo panali pamene mkazi anaona kuti anasiya chofunda chake m'dzanja lake, nathawira kubwalo,


ndipo panali pamene iye anamva kuti ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chofunda chake kwa ine nathawira kubwalo.


Ndipo ananena kwa iye monga mau awa, anati, Analowa kwa ine kapolo wa Chihebri uja, munabwera naye kwathu, kundipunza ine:


Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyake anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine.


chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m'dzenjemu.


Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji, lilime lonyenga iwe?


Mboni za chiwawa ziuka, zindifunsa zosadziwa ine.


chifukwa cha mau a mdani, chifukwa cha kundipsinja woipa; pakuti andisenza zopanda pake, ndipo adana nane mumkwiyo.


Wobisa udani ali ndi milomo yonama; wonena ugogodi ndiye chitsiru.


Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.


Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.


Okhala pafupi ndi okhala patali adzakuseka pwepwete, wodetsedwa dzina iwe, wodzala ndi kusokosera.


Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;


Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine.


Ndipo anayamba kumnenera Iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Khristu mfumu.


mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; monga osocheretsa, angakhale ali oona;


Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa