Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 38:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingachitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeze iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingachitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeza iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Yuda adati, “Zinthu zimenezo atenge zikhale zake, kuwopa kuti anthu angadzatiseke. Ngakhale sudampeze mkaziyo, komabe ine ndidaamtumizira ndithu mbuziyi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Pamenepo Yuda anati, “Mulekeni atenge zinthuzo zikhale zake, kuopa kuti anthu angatiseke. Ine sindinalakwe, ndinamutumizira kamwana kambuzika, koma simunamupeze.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 38:23
8 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeze mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano.


Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wachita chigololo, ndiponso taonani, ali ndi pakati ndi chigololocho. Ndipo Yuda anati, Mtulutse iye kuti amponye pamoto.


Chifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kuchita chimene chili choipa pamaso pake? Unakantha Uriya Muhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wake akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.


Adzalasidwa nanyozedwa; chitonzo chake sichidzafafanizidwe.


Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu zimene muchita nazo manyazi tsopano? Pakuti chimaliziro cha zinthu izi chili imfa.


koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.


pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi.


(Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.)


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa