Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 38:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeze mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeza mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Adabwerera kwa Yuda nakamuuza kuti, “Sindidampeze mkazi uja, ndipo anthu akumeneko andiwuza kuti, ‘Chikhalire sipadakhale mkazi wadama pa malo amenewo.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Choncho anabwerera kwa Yuda nati, “Sindinamupeze mkazi uja. Kuwonjeza apo, anthu a kumeneko amati, ‘Sipanakhalepo mkazi wadama pano.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 38:22
2 Mawu Ofanana  

Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? Ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano.


Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingachitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeze iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa