Genesis 38:18 - Buku Lopatulika18 Ndipo iye anati, Chikole chanji ndidzakupatsa iwe? Ndipo mkazi anati, Mphete yako, ndi chingwe chako, ndi ndodo ili m'dzanja lako. Ndipo anampatsa izo, nalowana naye, ndipo mkazi anatenga pakati ndi iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ndipo iye anati, Chikole chanji ndidzakupatsa iwe? Ndipo mkazi anati, Mphete yako, ndi chingwe chako, ndi ndodo ili m'dzanja lako. Ndipo anampatsa izo, nalowana naye, ndipo mkazi anatenga pakati ndi iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Yuda adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna chikole chotani?” Tamara adayankha kuti, “Mundipatse mphete yanu pamodzi ndi chingwe chanu chomwecho, ndi ndodo yanu yoyendera imene ili m'manja mwanuyi.” Yuda adapereka zonsezo kwa Tamara. Atatero Yuda adagona naye mkaziyo, ndipo adatenga pathupi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Iye anati, “Ndikupatse chikole chanji?” Mkaziyo anayankha, “Mundipatse mphete yanuyo, chingwe chanucho pamodzi ndi ndodo imene ili mʼdzanja lanulo.” Choncho anazipereka kwa iye nagona naye ndipo anatenga pathupi. Onani mutuwo |