Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 37:20 - Buku Lopatulika

20 Tiyeni tsopano timuphe iye timponye m'dzenje, ndipo tidzati, Wajiwa ndi chilombo; ndipo tidzaona momwe adzachita maloto ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Tiyeni tsopano timuphe iye timponye m'dzenje, ndipo tidzati, Wajiwa ndi chilombo; ndipo tidzaona momwe adzachita maloto ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Tiyeni timuphe, mtembo wake tiwuponye m'chitsime china mwa zitsime zili apazi. Tizikanena kuti wajiwa ndi chilombo, ndipo tidzaone tanthauzo lake la maloto ake aja.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Tsono tiyeni timuphe ndi kuponya thupi lake mu chimodzi mwa zitsime izi ndipo tidzati anadyedwa ndi nyama zakuthengo zolusa. Tsono timuonera zomwe ziti zichitike ndi maloto ake aja.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 37:20
25 Mawu Ofanana  

Ndipo anati wina ndi mnzake, Taonani, alinkudza mwini maloto uja.


Ndipo Yuda anati kwa abale ake, Nanga tidzapindulanji tikamupha mbale wathu ndi kufotsera mwazi wake?


natumiza malaya amwinjiro, nadza nao kwa atate ao: ndipo anati, Siwa tawatola; muzindikire tsono ngati ndi malaya a mwana wanu, kapena ndi ena.


Ndipo anazindikira nati, Ndiwo malaya a mwana wanga: wajiwa ndi chilombo: Yosefe wakadzulidwa ndithu.


Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Ine ndine Yosefe; kodi akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ake sanakhoze kumyankha iye; pakuti anavutidwa pakumuona iye.


Ndipo atachoka iye, mkango unakomana naye panjira, numupha ndipo mtembo wake unagwera m'njiramo, bulu naima pafupi, mkangonso unaima pafupi ndi mtembo.


Ndipo anacheuka, nawaona, nawatemberera m'dzina la Yehova. Ndipo kuthengo kunatuluka zimbalangondo ziwiri zazikazi, ndi kupwetedza mwa iwo ana makumi anai mphambu awiri.


Alimbikitsana m'chinthu choipa; apangana za kutchera misampha mobisika; akuti, Adzaiona ndani?


Mwananga, akakukopa ochimwa usalole.


pakuti mapazi ao athamangira zoipa, afulumira kukhetsa mwazi.


Wobisa udani ali ndi milomo yonama; wonena ugogodi ndiye chitsiru.


Kupweteka mtima nkwa nkhanza, mkwiyo usefuka; koma ndani angalakike ndi nsanje?


Wobisa machimo ake sadzaona mwai; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.


Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa;


Chifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tavomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga;


Ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupirira, mudzakhulupirira bwanji, ngati ndikuuzani za Kumwamba?


Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.


Ndipo tsono taona ndidziwa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndi kuti ufumu wa Israele udzakhazikika m'dzanja lako.


Ndipo Saulo ananyamuka, natsikira chipululu cha Zifi, ndi anthu zikwi zitatu a Israele osankhika, kukafuna Davide m'chipululu cha Zifi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa