Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 37:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo anati kwa iye, Pita tsopano, nukaone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta zili bwino; nundibwezere ine mau. Ndipo anamtuma iye kuchokera m'chigwa cha Hebroni, ndipo anadza ku Sekemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo anati kwa iye, Pita tsopano, nukaone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta zili bwino; nundibwezere ine mau. Ndipo anamtuma iye kuchokera m'chigwa cha Hebroni, ndipo anadza ku Sekemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Tsono bambo wakeyo adamuuza kuti, “Pita ukaŵaone abale ako m'mene aliri, ndiponso ngati zoŵeta zili bwino, kenaka udzandiwuze.” Choncho bambo wake adatuma Yosefe kuchokera ku chigwa cha Hebroni. Yosefe atafika ku Sekemu,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Choncho anati kwa iye, “Pita ukaone ngati abale ako ali bwino. Ukaonenso nkhosa ngati zili bwino. Kenaka ubwere udzandiwuze.” Choncho Israeli anatuma Yosefe kuchokera ku chigwa cha Hebroni. Yosefe atafika ku Sekemu,

Onani mutuwo Koperani




Genesis 37:14
22 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anasuntha hema wake nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure, imene ili mu Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.


Zitatha izi Abrahamu anaika Sara mkazi wake m'phanga la munda wa Makipela patsogolo pa Mamure (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani.


Ndipo Sara anafa mu Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire.


Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? Nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wake wamkazi alinkudza nazo nkhosa.


Ndipo Yakobo anafika kwa Isaki atate wake ku Mamure, ku Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni) kumene anakhala Abrahamu ndi Isaki.


Ndipo anampeza munthu, taonani, analinkusokera m'thengo; munthuyo ndipo anamfunsa, nati, Kodi ufuna chiyani?


Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.


Ndipo anafunsa iwo za ubwino wao, nati, Kodi atate wanu ali ndi moyo? Wokalamba uja amene munanena uja: kodi alipo?


Ndipo pakufika kwa iye Uriya uja, Davide anamfunsa kuti, Yowabu ali bwanji? Ndi anthu ali bwanji? Ndi nkhondo ili bwanji?


Ndipo mfumu inanena ndi Mkusiyo, Mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Mkusiyo nayankha, Adani a mbuye wanga mfumu, ndi onse akuukira inu kukuchitirani zoipa, akhale monga mnyamata ujayo.


Motero mwazi wao udzabweranso pamutu wake wa Yowabu, ndi pamutu wa mbumba yake, ku nthawi yamuyaya; koma Davide, ndi mbumba yake, ndi banja lake, ndi mpando wake wachifumu adzakhala ndi mtendere wa Yehova ku nthawi yamuyaya.


Ndi Mordekai akayendayenda tsiku ndi tsiku kubwalo la nyumba ya akazi, kuti adziwe umo akhalira Estere, ndi chimene chidzamchitikira.


Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele.


Nimufune mtendere wa mzinda umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wake inunso mudzakhala ndi mtendere.


Ndipo anakwera njira ya kumwera nafika ku Hebroni; ndi apa panali Ahimani, Sesai, ndi Talimai, ana a Anaki. (Koma atamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri ndipo anamanga Zowani mu Ejipito.)


nanena, Ukadazindikira tsiku ili, inde iwetu zinthu za mtendere! Koma tsopano zibisika pamaso pako.


Pamenepo Yoswa anamdalitsa, napatsa Kalebe mwana wa Yefune Hebroni likhale cholowa chake.


Chifukwa chake Hebroni likhala cholowa chake cha Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi mpaka lero lino; popeza anatsata Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wonse.


Koma kale dzina la Hebroni linali mzinda wa Araba, ndiye munthu wamkulu pakati pa Aanaki. Ndipo dziko linapumula nkhondo.


Ndipo Yuda anamuka kwa Akanani akukhala mu Hebroni; koma kale dzina la Hebroni ndilo mudzi wa Ariba; ndipo anakantha Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai.


Ndipo Davide anasiya akatundu ake m'dzanja la wosungira akatundu, nathamangira ku khamulo, nadza nawalonjera abale ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa