Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 36:18 - Buku Lopatulika

18 Amenewa ndi ana aamuna a Oholibama mkazi wake wa Esau; mfumu Yeusi, mfumu Yalamu, mfumu Kora, amenewa ndi mafumu obadwa kwa Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mkazi wake wa Esau.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Amenewa ndi ana amuna a Oholibama mkazi wake wa Esau; mfumu Yeusi, mfumu Yalamu, mfumu Kora, amenewa ndi mafumu obadwa kwa Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mkazi wake wa Esau.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau, panali mafumu aŵa: Yeusi, Yalamu ndi Kora. Ameneŵa ndiwo mafumu amene mkazi wa Esau, Oholibama mwana wa Ana, adabala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau munali mafumu awa: Yeusi, Yolamu, ndi Kora. Amenewa anali mafumu mwa ana a mkazi wa Esau, Oholibama, mwana wa Ana.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 36:18
6 Mawu Ofanana  

Ana aamuna a Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni, mkazi wake wa Esau, ndi awa: ndipo iye anambalira Esau Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora.


Amenewa ndi ana aamuna a Reuwele mwana wamwamuna wa Esau: mfumu Nahati, mfumu Zera, mfumu Sama, mfumu Miza; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Reuwele m'dziko la Edomu: amenewa ndi ana aamuna a Basemati mkazi wake wa Esau.


Amenewa ndi ana aamuna a Esau, amenewa ndi mafumu ao; yemweyo ndi Edomu.


Esau anatenga akazi ake a ana aakazi a mu Kanani: Ada mwana wamkazi wa Eloni Muhiti, ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni Muhivi;


ndipo Oholibama anabala Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora; amenewa ndi ana aamuna a Esau, amene anambadwira m'dziko la Kanani.


Ana a Esau: Elifazi, Reuwele, ndi Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa