Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 34:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwandisautsa ndi kundinukhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperizi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwandisautsa ndi kundinukhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperizi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Yakobe adauza Simeoni ndi Levi kuti, “Hi, mwandiputira nkhondo. Dzina langa laipa pakati pa anthu a dziko lino, Akanani ndi Aperizi. Ine ndilibe anthu ambiri, tsono iwoŵa akaitanizana kuti adzandithire nkhondo, ine ndi banja langa lonse, tonse pamodzi tidzaonongeka.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Pamenepo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, “Mwandiputira mavuto, ndi kundiyipitsira dzina pakati pa anthu a mʼdziko lino, Akanaani ndi Aperezi. Ife ndife owerengeka, ndipo atati aphatikizane kudzandithira nkhondo, ndiye kuti ine ndi banja langa tidzawonongeka.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 34:30
33 Mawu Ofanana  

ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aejipito, adzati, Uyu ndi mkazi wake: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo.


ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;


Ndipo Abramu anapitirira m'dzikomo kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m'dzikomo nthawi yomweyo.


Ndipo panali ndeu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti. Akanani ndi Aperizi ndipo analinkukhala nthawi yomweyo m'dzikomo.


Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.


ndi chuma chao chonse ndi ana ao ndi akazi ao anawagwira, nafunkha zonse za m'nyumba.


Ndipo iwo anati, Kodi iye ayenera kusandutsa mlongo wathu wadama?


Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo mu Ejipito, amene anatuluka m'chuuno mwake, pamodzi ndi akazi a ana aamuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi;


ndi ana aamuna a Yosefe, amene anambadwira iye mu Ejipito ndiwo anthu awiri; anthu onse a mbumba ya Yakobo, amene analowa mu Ejipito anali makumi asanu ndi awiri.


Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Beterehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu chikwi chimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.


Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Mulowe kwa akazi aang'ono a atate wanu amene iye anawasiya kuti asunge nyumbayo; ndipo Aisraele onse adzamva kuti atate wanu aipidwa nanu; pomwepo manja a onse akukhala nanu adzalimba.


Ndipo iye anali mdani wa Israele masiku onse a Solomoni, kuonjezerapo choipa anachichita Hadadi, naipidwa nao Aisraele, nakhala mfumu ya ku Aramu.


Nati iye, Sindimavute Israele ine ai, koma inu ndi nyumba ya atate wanu; popeza munasiya malamulo a Yehova, ndi kutsata Abaala.


Kumbukirani zodabwitsa zake adazichita, zizindikiro zake, ndi maweruzo a pakamwa pake.


Pokhala inu anthu owerengeka, inde anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo;


Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, Hanuni ndi ana a Amoni anatumiza matalente chikwi chimodzi a siliva, kudzilembera magaleta ndi apakavalo ku Mesopotamiya, ndi ku Aramu-Maaka, ndi ku Zoba.


Ndi ana a Karimi: Akara wovuta Israeleyo, amene analakwira choperekedwa chiperekerecho.


pokhala iwo anthu owerengeka, inde, anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo;


ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndi kuwapatsa lupanga m'dzanja lao kutipha nalo.


Wachifundo achitira moyo wake zokoma; koma wankhanza avuta nyama yake.


Wovuta banja lake adzalowa m'zomsautsa; wopusa adzatumikira wanzeru.


Wopindula monyenga avuta nyumba yake; koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.


mafanidwe a nyama iliyonse ili padziko lapansi, mafanidwe a mbalame iliyonse yamapiko yakuuluka m'mlengalenga,


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang'ono mwa amitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao.


Yehova sanakondwere nanu, ndi kukusankhani chifukwa cha kuchuluka kwanu koposa mitundu ina yonse ya anthu, kapena kuchepera kwanu;


Ndipo Yoswa anati, Watisautsiranji? Yehova adzakusautsa lero lino. Ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nawatentha ndi moto, nawaponya miyala.


Ndipo Aisraele onse anamva kunena kuti Saulo anathyola kaboma ka Afilisti, ndi kuti Afilisti anyansidwa ndi Aisraele. Ndipo anthuwo anasonkhana kwa Saulo ku Giligala.


Ndipo Samuele anati, Ndikamuka bwanji? Saulo akachimva, adzandipha. Ndipo Yehova anati, Umuke nayo ng'ombe yaikazi, nunene kuti, Ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova.


Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake.


Ndipo Akisi anakhulupirira Davide, nati, Anadziipitsa ndithu pakati pa anthu a Israele, chifukwa chake iye adzakhala mnyamata wanga chikhalire.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa