Genesis 34:25 - Buku Lopatulika25 Ndipo panali tsiku lachitatu pamene anamva kuwawa, ana aamuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ake a Dina, anatenga wina lupanga lake wina lake, nalimbika mtima nalowa m'mzinda napha amuna onse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 Ndipo panali tsiku lachitatu pamene anamva kuwawa, ana amuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ake a Dina, anatenga wina lupanga lake wina lake, nalimbika mtima nalowa m'mudzi napha amuna onse. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Patangopita masiku atatu, zilonda za kuumbala kuja zisanapole pa anthu aja, ana aŵiri a Yakobe, Simeoni ndi Levi, alongo ake a Dina, adatenga mikondo yao, nakaloŵa mosadziŵika mumzinda muja, nkukapha amuna onse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Patapita masiku atatu, amuna onse akumvabe ululu wa kuchita mdulidwe uja, ana awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, alongo ake a Dina, anatenga malupanga ndi kulowa mu mzindawo mwakachetechete napha amuna onse. Onani mutuwo |
Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka mu Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.