Genesis 34:21 - Buku Lopatulika21 Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; chifukwa chake akhale m'dzikomo, achite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikolo lili lalikulu lokwanira iwo; tidzitengere ana ao aakazi akhale aakazi athu, tiwapatse amenewa ana athu aakazi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201421 Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; chifukwa chake akhale m'dzikomo, achite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikolo lili lalikulu lokwanira iwo; tidzitengere ana ao akazi akhale akazi athu, tiwapatse amenewa ana athu akazi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa21 “Anthu aŵa ndi abwenzi athu. Motero tiŵalole kuti akhale m'dziko mwathu muno, kuti azichita malonda mwaufulu. Dzikoli ndi lalikulu ndipo lingathenso kuŵakwanira iwowo. Tiyeni tizikwatirana nawo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero21 Iwo anati, “Anthu awa ndi a mtendere. Aloleni kuti akhale mʼdziko mwathu muno nachitamo malonda. Dzikoli lili ndi malo ambiri woti iwo nʼkukhalamo. Tingathe kukwatira ana awo aakazi ndipo angathe kukwatira ana athu aakazi. Onani mutuwo |