Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 34:22 - Buku Lopatulika

22 Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Komatu anthu ameneŵa adzavomera kukhala pakati pathu ndi kusakanizana nafe, kuti tikhale mtundu umodzi, pokhapokha ifeyo tikaumbala amuna onse monga amachitira iwowo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Komatu anthuwa adzavomereza kukhala amodzi a ife pokhapokha ngati amuna onse pakati pathu atachita mdulidwe monga alili iwo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 34:22
3 Mawu Ofanana  

Ili ndi pangano langa limene uzisunga pakati pa Ine ndi iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu.


Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; chifukwa chake akhale m'dzikomo, achite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikolo lili lalikulu lokwanira iwo; tidzitengere ana ao aakazi akhale aakazi athu, tiwapatse amenewa ana athu aakazi.


Kodi ng'ombe zao ndi chuma chao ndi zoweta zao sizidzakhala zathu? Pokhapo tivomerezana nao ndipo adzakhala pamodzi ndi ife.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa